Tate wa fuko la Malawi Dr Lazarus McCarthy Chakwera wafunila zabwino team ya Malawi pamene ikusewera mpira wa mchembere mbaya mwa mnanu wa dziko lose lapansi ku South Africa.
Polankhula izi ku nyumba ya chifumu, a Chakwera ati ndipofunika kuti team ya ma Queens ipambane ma sewera ake chifukwa team imeneyi imatchuka ndi kuwina nthawi zonse.
A Chakwera poyankhura kudzera pa makina a internet anati iwo ndi boma lawo apitiliza kupempherera team imeneyi.
Ma Queens anayankha pamakina pomwepo kuthokoza mtsogoleriyu kamba kopeza nthawi yofunira zabwino atsikanawa omwe akhala akuchita bwino. Mwachitsanzo tikunena pano iwo agonjetsa kale ma Team a Scotland, Barbados ndi Fiji ku Cape Town komweko.